28 Ndiyeno anthu ena onse, ansembe,+ Alevi,+ alonda a pazipata,+ oimba,+ Anetini,+ ndi aliyense amene anadzipatula kwa mitundu ya anthu a m’mayikowo+ kuti asunge chilamulo+ cha Mulungu woona, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi ndi aliyense wodziwa zinthu ndi wozindikira,+