8 Ngati mungandikomere mtima mfumu+ ndipo ngati zingakukomereni kuchita zimene ndapempha n’kundipatsa zimene ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzerani mawa. Ndipo mawa ndidzanena pempho langa monga mmene inu mfumu mwanenera.”+