-
Esitere 1:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Choncho mfumu inalemba makalata ndi kuwatumiza+ m’zigawo zonse za ufumu wake. Chigawo chilichonse+ anachilembera kalata malinga ndi mmene anthu a kumeneko amalembera ndiponso malinga ndi chinenero chawo. Anachita izi kuti mwamuna aliyense apitirize kutsogolera banja lake monga mutu,+ ndiponso kuti banjalo lizilankhula chinenero cha anthu a mtundu wa mwamunayo.
-
-
Esitere 3:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Kenako anaitana alembi a mfumu+ m’mwezi woyamba, pa tsiku la 13 la mweziwo. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a m’zigawo zosiyanasiyana+ za ufumuwo ndi akalonga a anthu osiyanasiyana m’chigawo chilichonse. Makalata amenewa anawalemba malinga ndi mmene anthu a m’chigawo chilichonse anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo. Makalatawa anawalemba m’dzina+ la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yake yodindira.+
-