7 Moredekai ndi amene analera+ Hadasa, amene ndi Esitere, mwana wa m’bale wa bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndi wokongola kwambiri.+ Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredekai anam’tenga ngati mwana wake.