3 “Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mwakhala bwinja+ ndipo adani anu akulumani kumbali zonse.+ Izi zachitika kuti anthu otsala a mitundu ina akutengeni kuti mukhale awo.+ Anthu akunena za inu ndi pakamwa pawo+ ndipo akukunenerani zoipa.+