Salimo 22:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Koma ine ndine nyongolotsi+ osati munthu.Anthu amanditonza ndipo ndine wonyozeka kwa anthu.+ Luka 17:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake.+ Tangochita zimene tinayenera kuchita.’” Luka 18:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+ 1 Petulo 5:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.+
10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake.+ Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”
13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+