Yesaya 53:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+ Mateyu 27:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Atam’pachika+ anagawana malaya ake akunja+ mwa kuchita maere,+ Yohane 20:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+
7 Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+
25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+