Yoswa 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+ Salimo 25:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake,+Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.+ Yakobo 1:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Choncho ngati wina akusowa nzeru,+ azipempha kwa Mulungu,+ ndipo adzamupatsa,+ popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.+
7 “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+
5 Choncho ngati wina akusowa nzeru,+ azipempha kwa Mulungu,+ ndipo adzamupatsa,+ popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.+