28 Iwo anenepa+ ndipo matupi awo asalala. Achitanso zinthu zoipa zosawerengeka. Iwo sanaweruze mlandu wa munthu aliyense mwachilungamo,+ ngakhale mlandu wa mwana wamasiye,+ pofuna kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Iwo sanachitire chilungamo munthu wosauka.’”