-
Nehemiya 5:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Tsiku lililonse ndinali kuuza anthu kuti akonze ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa zosankhidwa mwapadera 6 ndi mbalame. Ndipo kamodzi pa masiku 10 alionse ndinali kupereka vinyo wochuluka wamtundu uliwonse.+ Kuwonjezera pamenepo, sindinapemphe kuti andipatse chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa chifukwa utumiki umene anthuwa anali kuchita unali wolemetsa.
-
-
Esitere 1:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Masiku amenewa atatha, mfumu inakonza phwando la masiku 7 m’munda wamaluwa, pabwalo la nyumba yake. Phwandoli inakonzera anthu onse okhala kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani, anthu olemekezeka ndi anthu wamba omwe.
-