32Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anakhala ndi ziweto zambiri, zankhaninkhani. Iwo anayamba kusirira dziko la Yazeri+ ndi la Giliyadi, ndipo deralo linalidi malo abwino a ziweto.
12 Choncho pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu. Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa Aroweli,+ mzinda umene uli m’chigwa cha Arinoni, ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi, ndi mizinda yake.