16 Zofunkha zake zonse muzizisonkhanitsa pakati pa bwalo la mzindawo. Pamenepo muzitentha mzindawo+ ndi zofunkha zake zonse monga nsembe yathunthu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Ndipo mzindawo uzikhala bwinja mpaka kalekale.+ Usadzamangidwenso.