7 “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+