17 Kenako mfumu ya Asuri+ inatuma Tatani,+ Rabisarisi, ndi Rabisake+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inawatumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iwo anapitadi n’kukaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+