8 Choncho iye anaima n’kuyamba kufuulira asilikali a Isiraeli+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo? Ine ndabwera kudzamenyera nkhondo Afilisiti. Inuyo ndinu antchito+ a Sauli. Ndiye sankhani munthu woti amenyane nane, ndipo abwere kuno.