2 Kenako Mulungu anauza munthu amene anavala zovala zansalu+ uja, kuti: “Pita pakati pa mawilo,+ pansi pa akerubi. Ukatengepo makala+ amoto odzaza manja ako onse awiri kuchokera pakati pa akerubiwo, ndipo ukawaponye pamzindawo.”+ Chotero iye anapitadi ine ndikuona.