2 “Kulitsa hema wako.+ Nsalu za hema wako wamkulu zitambasulidwe. Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za hema wako ndipo ulimbitse zikhomo zake.+
6 Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.+ Anthu adzakutchani atumiki+ a Mulungu wathu.+ Mudzadya zinthu zochokera ku mitundu ya anthu+ ndiponso mudzalankhula za inuyo mokondwera, chifukwa cha chuma ndi ulemerero zimene mudzapeze kwa mitunduyo.+
7 “‘Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.+ Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero,’+ watero Yehova wa makamu.