6 Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.+ Anthu adzakutchani atumiki+ a Mulungu wathu.+ Mudzadya zinthu zochokera ku mitundu ya anthu+ ndiponso mudzalankhula za inuyo mokondwera, chifukwa cha chuma ndi ulemerero zimene mudzapeze kwa mitunduyo.+
11 chifukwa mudzayamwa bere lake ndipo mudzakhuta kutonthoza kwake. Komanso mudzayamwa mkaka wake ndipo mudzasangalala kwambiri ndi bere lake laulemerero.+