18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi chilombo chakuthengo,+ cholengedwa chouluka m’mlengalenga ndi cholengedwa chokwawa panthaka, kuti ndithandize anthu anga. Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo padziko.+ Pamenepo ndidzawachititsa kukhala mwabata.+