11 Koma inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti musonkhanitsidwe ngati pa nthawi yokolola yakhazikitsidwa. Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.”+
13 “Yambani kumweta ndi chikwakwa,+ pakuti zokolola zacha.+ Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri.+