13 Pakuti milungu yako, iwe Yuda,+ yafanana ndi mizinda yako kuchuluka kwake. Ndipo chinthu chochititsa manyazi+ mwachimangira maguwa ansembe, anthu inu. Mwachimangira maguwa ansembe ochuluka mofanana ndi misewu ya mu Yerusalemu. Mwamanga maguwa ansembe kuti muzifukizira Baala nsembe zautsi.’+