25 Ndiyeno Palali mwana wamwamuna wa Uzai, anakonza mpandawo kutsogolo kwa Mchirikizo wa Khoma ndipo anakonzanso nsanja yochokera pa Nyumba ya Mfumu+ imene ili kumtunda m’Bwalo la Alonda.+ Kenako, Pedaya mwana wamwamuna wa Parosi,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Palali analekezera.