3 Anayenda m’njira ya mafumu a ku Isiraeli,+ ndipo ngakhale mwana wake wamwamuna anamuwotcha* pamoto,+ mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa chifukwa cha ana a Isiraeli.
9 Koma Manase+ anapitiriza kunyengerera Yuda+ ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.+