11 “Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka, ndipo ndikuganizira zokuchitani chinthu choipa.+ Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.”’”+