4 Pamenepo akalonga anayamba kuuza mfumu kuti: “Chonde lolani kuti munthu uyu aphedwe,+ chifukwa iye akufooketsa amuna ankhondo amene atsala mumzinda uno, pamodzi ndi anthu onse, mwa kuwauza mawu amenewa.+ Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.”