3 Tsopano iweyo mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo ndipo upite ku ukapolo masana, anthu akuona. Upite ku ukapolo iwo akuona. Uchoke kwanu kupita kumalo ena. Mwina azindikira tanthauzo lake ngakhale kuti iwo ndi anthu opanduka.+