1 Tsopano awa ndiwo masomphenya a Obadiya:
Zimene Yehova Ambuye Wamkulu Koposa wanena zokhudza Edomu ndi izi:+ “Ife tamva uthenga wochokera kwa Yehova ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti: ‘Nyamukani anthu inu, tiyeni timuukire ndi kumenyana naye.’”+