23 Kenako iye anapanga thanki yamkuwa.+ Pakamwa pa thankiyo panali papakulu mikono 10 kuyeza modutsa pakati pake, ndipo panali pozungulira. Thankiyo inali yaitali mikono isanu kuchokera pansi kufika pamwamba. Pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira thankiyo.+