19 Ndinakupatsa chakudya choti uzidya. Ndinakupatsa ufa wosalala, mafuta, ndi uchi.+ Koma zinthu zimenezi, iwe unaziika pamaso pa zifanizirozo kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi,+ ndipo unapitiriza kuchita zimenezi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”