-
Genesis 13:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.
-
-
Ezekieli 28:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu.+ Unali kuvala chovala chokongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse monga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi,+ yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi. Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide. Anakukonzera zimenezi pa tsiku limene unalengedwa.
-