Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.+ Chikumbutso. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
80 Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+
Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+
Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+
2 Sonyezani mphamvu zanu pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase,+
Ndipo bwerani mudzatipulumutse.+
3 Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+
Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+
4 Inu Yehova Mulungu wa makamu, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?+
5 Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,+
Ndipo mukuwamwetsabe misozi yochuluka kwambiri.+
6 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azimenyana polimbirana ifeyo.+
Ndipo adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+
7 Inu Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+
Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+
8 Munachititsa mtengo wa mpesa kuchoka mu Iguputo.+
Munapitikitsa mitundu ya anthu kuti mubzalemo mtengowo.+
9 Munalambula malo obzalapo mtengo wa mpesawo+ kuti uzike mizu ndi kudzaza dziko.+
10 Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake,
Ndipo mikungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.+
11 Pang’onopang’ono nthambi zake zinafika kunyanja,+
Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.+
12 N’chifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wake wamiyala?+
Ndipo n’chifukwa chiyani anthu onse odutsa mumsewu akuthyola zipatso zake?+
13 Nguluwe ikuwononga mtengowo,+
Ndipo magulu a nyama zakutchire akuudya.+
14 Inu Mulungu wa makamu, chonde bwererani.+
Yang’anani pansi pano muli kumwambako, ndipo onani ndi kusamalira mtengo wa mpesa uwu.+
15 Onani muzu umene dzanja lanu lamanja linabzala.+
Muonenso mwana wanu amene munamulimbitsa kuti inu mulemekezeke.+
16 Watenthedwa ndi moto ndi kudulidwa.+
Iwo amawonongeka ndi kudzudzula kwa pankhope panu.+
17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa kudzanja lanu lamanja,+
Ndipo likhale pa mwana wa munthu amene mwamulimbitsa kuti mulemekezeke.+
18 Ndipo ife sitidzabwerera kukusiyani.+
Tisungeni amoyo kuti tiitane pa dzina lanu.+
19 Inu Yehova Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+
Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+