4 Motero anthuwo anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa makamu, amene akukhala pa akerubi.+ Ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anali pamenepo ndi likasa la pangano la Mulungu woona.+
2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+