9 Tsopano m’chaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, kutanthauza chaka cha 7 cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Salimanesere+ mfumu ya Asuri anabwera ku Samariya n’kuzungulira mzindawo.+
32Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa ntchito zokhulupirika+ za Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera n’kudzazungulira Yuda ndipo anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Iye anali kuganiza zogonjetsa mizindayo kuti ikhale yake.