25 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+