18 Munthu uja anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Amenewa ndi malamulo a guwa lansembe amene anaperekedwa pa nthawi imene analipanga. Guwali analipanga kuti aziperekerapo nsembe zopsereza zathunthu+ ndi kuwazapo magazi.’+