Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 12:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Nkhosa yanuyo ikhale yopanda chilema,+ yamphongo, yachaka chimodzi.+ Mungatenge mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi.

  • Levitiko 22:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nyama iliyonse yachilema musaipereke nsembe,+ chifukwa Mulungu sadzakuyanjani.

  • Deuteronomo 15:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+

  • Malaki 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Aliyense wochita zachinyengo popereka nsembe nyama yachilema ndi wotembereredwa. Iye amalonjeza ndi kupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova pamene nyama yamphongo yabwinobwino, ali nayo pagulu la ziweto zake.+ Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

  • Aheberi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo?

  • 1 Petulo 1:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali,+ monga a nkhosa yopanda chilema ndi yopanda mawanga,+ magazi a Khristu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena