19 Tsopano akerubi aja anatambasula mapiko awo n’kunyamuka kuchoka pansi+ ine ndikuona. Atanyamuka, mawilo aja anali pambali pawo. Kenako iwo anakaima pakhomo la kum’mawa la chipata cha nyumba ya Yehova, ndipo ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo.