7 Tsopano Yosiya anapereka kwa ana a anthuwo ziweto zokwana 30,000, zomwe zinali ana a nkhosa amphongo ndi ana a mbuzi amphongo. Anapereka zonsezo kuti zikhale nyama zophera pasika za onse amene analipo, ndiponso ng’ombe 3,000.+ Zonsezi zinachokera pa katundu wa mfumu.+