-
Ezekieli 48:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 “Mayina a mafuko ndi awa. Fuko la Dani+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kumalire a kumpoto a dzikolo, m’mbali mwa msewu wa ku Heteloni+ wopita kumalire a Hamati.+ Malire a gawolo chakumpoto, akafikenso ku Hazara-enani,+ kumalire a Damasiko kufupi ndi Hamati. Gawolo likhale ndi malire kumbali ya kum’mawa ndi kumbali ya kumadzulo.
-