10 Ndinapitiriza kuona masomphenya, ndipo ndinaona kuti pamwamba pa thambo+ limene linali pamwamba pa mitu ya akerubi, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro.+ Chinthucho chinalinso chooneka ngati mpando wachifumu,+ ndipo chinali kuonekera pamwamba pa mitu yawo.