24 Wakhala ngati mbidzi+ yaikazi yozolowera kukhala m’chipululu imene ili ndi chilakolako champhamvu, imene ikupuma mwawefuwefu.+ Ndani angaibweze pa nthawi yake yokweredwa? Mbidzi zamphongo zoifunafuna sizidzavutika kuipeza. M’mwezi wake wokweredwa zidzaipeza.