4 Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha m’buku la Mose,+ chimene Yehova analamula kuti: “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana,+ ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+