10 Inuyo mfumu munaika lamulo lakuti munthu aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ agwade ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo alambire fano lagolide.