Danieli 7:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 “Pambuyo pa zimenezi, ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku*+ koma chinali ndi mapiko anayi a mbalame pamsana pake. Chilombochi chinali ndi mitu inayi+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro. Danieli 8:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamene ndinali kuganizira zimenezi, ndinangoona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kolowera dzuwa kudutsa padziko lonse lapansi koma sinali kukhudza pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+ Danieli 8:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+
6 “Pambuyo pa zimenezi, ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku*+ koma chinali ndi mapiko anayi a mbalame pamsana pake. Chilombochi chinali ndi mitu inayi+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro.
5 Pamene ndinali kuganizira zimenezi, ndinangoona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kolowera dzuwa kudutsa padziko lonse lapansi koma sinali kukhudza pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+
21 Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+