10 Koma nayenso No-amoni anayenera kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo. Ana ake anaphwanyidwaphwanyidwa m’misewu yake yonse+ ndipo anthu ake olemekezeka anawachitira maere.+ Anthu ake onse otchuka anamangidwa m’matangadza.+