20 “N’chifukwa chiyani mukundibweretsera lubani wochokera ku Sheba+ ndi mabango onunkhira ochokera kudziko lakutali? Zimenezi zili ndi ntchito yanji kwa ine? Nsembe zanu zopsereza zathunthu sizikundisangalatsa,+ ndipo nsembe zina zonse zimene mukupereka sizikundikondweretsa.”+