30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+
6 Zimenezi zachokera ku Isiraeli.+ Mmisiri ndiye anapanga fano la mwana wa ng’ombe la ku Samariya.+ Fanolo si Mulungu woona, chifukwa lidzangokhala ngati nkhuni zowazawaza.+