42 Koma ngakhale pamene anali kufika naye kwa iye, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kum’tsalimitsa mwamphamvu. Yesu anakalipira mzimu wonyansawo ndi kuchiritsa mnyamatayo. Kenako anamupereka kwa bambo ake.+
9 Koma pamene Mikayeli+ mkulu wa angelo+ anasemphana maganizo+ ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose,+ sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza,+ m’malomwake anati: “Yehova akudzudzule.”+