21 Atalengeza uthenga wabwino mumzinda umenewo ndi kuphunzitsa anthu angapo kuti akhale ophunzira,+ anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya.
16 Koma ophunzira ena a ku Kaisareya+ ananyamuka nafe, kuti atiperekeze kunyumba ya munthu wina kuti tikafikire kumeneko. Munthu ameneyu dzina lake linali Mnaso wa ku Kupuro, ndipo anali mmodzi wa ophunzira oyambirira.