Yesaya 47:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa. Mateyu 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa+ ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo.
13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa.
9 Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa+ ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo.